Check out the new design

《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 * - 译解目录


含义的翻译 章: 伊斯拉仪   段:
۞ قُلۡ كُونُواْ حِجَارَةً أَوۡ حَدِيدًا
Nena: “Khalani miyala kapena zitsulo.”
阿拉伯语经注:
أَوۡ خَلۡقٗا مِّمَّا يَكۡبُرُ فِي صُدُورِكُمۡۚ فَسَيَقُولُونَ مَن يُعِيدُنَاۖ قُلِ ٱلَّذِي فَطَرَكُمۡ أَوَّلَ مَرَّةٖۚ فَسَيُنۡغِضُونَ إِلَيۡكَ رُءُوسَهُمۡ وَيَقُولُونَ مَتَىٰ هُوَۖ قُلۡ عَسَىٰٓ أَن يَكُونَ قَرِيبٗا
“Kapena cholengedwa chilichonse mwa zomwe zikuoneka kuti nzovuta kwambiri m’mitima mwanu (m’maganizo mwanu), (ngakhale mutakhala zimenezo, mudzaukitsidwa).” Pamenepo anena: “Ndani adzatibweza?” Nena: “Yemwe adakulengani pachiyambi.” Pamenepo adzakupukusira mitu yawo ndi kunena: “Zichitika liti zimenezo?” Nena: “Mwina zili pafupi!”
阿拉伯语经注:
يَوۡمَ يَدۡعُوكُمۡ فَتَسۡتَجِيبُونَ بِحَمۡدِهِۦ وَتَظُنُّونَ إِن لَّبِثۡتُمۡ إِلَّا قَلِيلٗا
“(Zidzakhala) pa tsiku lomwe adzakuitanani (Allah), ndipo inu mudzayankha momuyamikira, ndipo mudzaganizira kuti simudakhale (pa dziko lapansi) koma (kwa) nthawi yochepa.”
阿拉伯语经注:
وَقُل لِّعِبَادِي يَقُولُواْ ٱلَّتِي هِيَ أَحۡسَنُۚ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ يَنزَغُ بَيۡنَهُمۡۚ إِنَّ ٱلشَّيۡطَٰنَ كَانَ لِلۡإِنسَٰنِ عَدُوّٗا مُّبِينٗا
Ndipo auze akapolo Anga kuti (nthawi zonse) azinena zomwe zili zabwino; chifukwa satana amakhwirizira mikangano pakati pawo; ndithu satana kwa munthu, ndi m’dani woonekera.
阿拉伯语经注:
رَّبُّكُمۡ أَعۡلَمُ بِكُمۡۖ إِن يَشَأۡ يَرۡحَمۡكُمۡ أَوۡ إِن يَشَأۡ يُعَذِّبۡكُمۡۚ وَمَآ أَرۡسَلۡنَٰكَ عَلَيۡهِمۡ وَكِيلٗا
Mbuye wanu akukudziwani bwino. Ngati afuna akuchitirani chisoni (mukatembenukira kwa Iye), ndipo ngati afuna, akulangani (mukapitiriza kumnyoza); ndipo sitidakutumize kuti ukhale muyang’anili wawo.
阿拉伯语经注:
وَرَبُّكَ أَعۡلَمُ بِمَن فِي ٱلسَّمَٰوَٰتِ وَٱلۡأَرۡضِۗ وَلَقَدۡ فَضَّلۡنَا بَعۡضَ ٱلنَّبِيِّـۧنَ عَلَىٰ بَعۡضٖۖ وَءَاتَيۡنَا دَاوُۥدَ زَبُورٗا
Ndipo Mbuye wako akuwadziwa bwino onse ali kumwamba ndi pansi, ndithu tawapatsa ulemelero wambiri aneneri ena kuposa ena. Ndipo Daud tidampatsa Zaburi.
阿拉伯语经注:
قُلِ ٱدۡعُواْ ٱلَّذِينَ زَعَمۡتُم مِّن دُونِهِۦ فَلَا يَمۡلِكُونَ كَشۡفَ ٱلضُّرِّ عَنكُمۡ وَلَا تَحۡوِيلًا
Nena: “Aitaneni amene mukuwatcha kuti ndi milungu kusiya Iye (Allah) kuti akuchotsereni masautso, sadzatha kukuchotserani vuto lililonse ngakhale kulisintha (kuti likhale chabwino).”
阿拉伯语经注:
أُوْلَٰٓئِكَ ٱلَّذِينَ يَدۡعُونَ يَبۡتَغُونَ إِلَىٰ رَبِّهِمُ ٱلۡوَسِيلَةَ أَيُّهُمۡ أَقۡرَبُ وَيَرۡجُونَ رَحۡمَتَهُۥ وَيَخَافُونَ عَذَابَهُۥٓۚ إِنَّ عَذَابَ رَبِّكَ كَانَ مَحۡذُورٗا
Iwo amene akuwapempha (naonso) akufunafuna njira yoziyandikitsira kwa Mbuye wawo (ngakhale) omwe ali pafupi mwa iwo (ndi Allah, monga angelo); naonso akuyembekezera chifundo chake ndi kuopa chilango chake; ndithu chilango cha Mbuye wako, nchoopedwa.
阿拉伯语经注:
وَإِن مِّن قَرۡيَةٍ إِلَّا نَحۡنُ مُهۡلِكُوهَا قَبۡلَ يَوۡمِ ٱلۡقِيَٰمَةِ أَوۡ مُعَذِّبُوهَا عَذَابٗا شَدِيدٗاۚ كَانَ ذَٰلِكَ فِي ٱلۡكِتَٰبِ مَسۡطُورٗا
Ndipo sipadzapezeka mudzi uliwonse koma Ife tidzauphwasula tsiku la Qiyâma lisanadze, kapena tidzaulanga ndi chilango chaukali (ngati uli woyenerana ndi zimenezo). Izi zidalembedwa m’buku.
阿拉伯语经注:
 
含义的翻译 章: 伊斯拉仪
章节目录 页码
 
《古兰经》译解 - 契瓦语翻译 - 哈利德·伊布拉欣·比德拉。 - 译解目录

由哈利德·伊布拉欣·白塔拉翻译。

关闭